HIS EXCELLENCY DR LAZARUS MCCARTHY CHAKWERA.

Chakwera anthu amamuziwa ngati munthu odekha osakonda zolakhulalakhul<br>a,munthu owopa Mulungu,munthu okwanilisa lonjezo lake komanso munthu okonda anthu osayang'ana mbali. Chinaso chodabwsa ndi chakuti a MEC atanena kuti a Chakwera apambana a Chakwera asayambe kunyadila anayamba Kaye kupemphera kuthokoza Mulungu ndipo post yawo yawo pa page pa FB Iwo anati "Zikomo ambuye wanga,Yesu" zomwe zikupasa anthu chiyembekezo kuti President ameneyi ndiwoopa Mulungu ndipo akwanisa zofuna zawo. Chakwera akhala President wa number 6 wadziko la Malawi ndipo alamulira kwa zaka zisanu 2020-2025.. A Chakwera amakondaso mpira ndipo amasapota Mighty Be forward Wanderers komanso Arsenal.

***   386 *** ***  4

Lazarus Chakwera ndi President wadziko la Malawi kuyambila pa *27 June,2020.* President number 6 wadziko la Malawi. Lero Malawitunes by public demand yapemphedwaso kuti iposite mbiri ya President wathu lero. Mulore kuti tilowe muthumba tisakanize zimenezi..

 

Lazarus McCarthy Chakwera adabadwa pa 5 April, 1955 (zaka 65 pano). Iye adabadwira mumzinda wa Lilongwe (chigawo chapakati m'dziko la Malawi). Chakwera bambo ake anachokera ku Dowa ndipo mayi ake adali a ku Mchinji. Chakwera ndi m'modzi mwa anthu andale a m'dziko la Malawi, yemwe ndi president wadziko la Malawi komanso wakhala mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) kuyambira m'chaka cha 2013, (chomwenso ndi chipani chachikulu m'dziko la Malawi). Lazarus Chakwera, adali mtsogoleri wambali yotsutsa boma m'nyumba yamalamulo. Iye, adakhalaponso mtsogoleri wa mpingo wa "Malawi Assemblies of God" kuyambira m'chaka cha 1989 kufikira pa 14 May, 2013 pamene adabwera poyera nkulengedza kuti watula pansi udindowu.

HIS EARLY LIFE.

Lazarus adabadwira mu mzinda wa Lilongwe m'banja lomwe makolo ake adali alimi (He was born to a subsistence farmer in the outskirt of Lilongwe city),kwao makolo awo anali ovutika kwambiri. Ana awiri aamuna omwe adabadwa koyambilira m'banjali, adamwalira adakali achichepere malinga ndi kukula kwa imfa za ana akhanda m'dziko la Malawi munthawiyo.
Dzina la Lazarus, akuti adapereka ndi bambo ake ndichikhulupiliro choti mwana uyu akhala moyo, saamwalira ngati ana enawo (potengera nkhani ya m'baibulo, yomwe imakamba za Lazaro yemwe adaukitsidwa kwaakufa ndi Yesu Khristu).
Lazarus, ndi mwana yekhayo wammuna yemwe adakali moyo kubanja kwawo, pamodzi ndi azichemwali ake.

Image

MAPHUNZIRO AWO

Lazarus Chakwera primary yake standard 1-4 adaphunzra Ku Malembo Primary school ndipo standard 5-7 adaphunzira Ku Nambuma primary school, Standard 8 adabwelera Ku Malembo komwe kuja ndipo adakhoza bwno kwambiri zomwe zinapangsa kuti amusankhile Ku Mtendere secondary school. Malingana ndi akubanja ake anati Chakwera from Standard 1 kufikira form 4 iyeyu samatuluka mu top 5 ya ana okhoza bwno. Atakhoza bwno mayeso a form 4 (MSCE) Chakwera adasankhidwa kupita Ku University of Malawi,Chancellor College.

M'chaka cha 1977, Chakwera adamalidza maphunziro a Bachelor of Arts (Philosophy) Degree from the University of Malawi,Chancellor Collge. Chakwera Adapedzanso honours degree (BTh) from the University of the North, Sovenga, South Africa. Mu 1991, iye adapedza masters (MTh), from the University of South Africa. M'chaka cha 2000, Chakwera adalandira doctorate (D. Min) kuchokera ku Trinity International University, in Deerfield, Illinois, USA. Mu 2005, "Pan Africa Theological Seminary" idapereka u Professor kwa a Chakwera (awarded him Professorship).

ACHIEVEMENTS .
Lazarus Chakwera, adagwirapo ntchito ngati instructor ku Assemblies of God School of Theology kuchokera m'chaka cha 1983 mpaka 2000. Adakali mkatikati mwa ntchitoyi, iye adasankhidwa kukhala Principal wasukuluyi mu 1996, ndipo Chakwera, wakhalanso ali co-director komanso lecturer ku "All Nations Theological Seminary".
Kuchoka m'chaka cha 1989 Chakwera wakhala akutsogolera mpingo wa Malawi Assemblies of God, ndipo pa 14 April, 2013, adabwera poyera nkulengedza khumbo lake lofuna kupikisana nawo pampando wa u president ku convention ya chipani chachikulu chotsutsa boma m'dziko la Malawi (MCP). Chakwera adapambana ndi mavoti ambiri ku convention_yo kuposa m'mene adapambanira mtsogoleri aliyense pa convention mu mbiri ya dziko la Malawi.

Image

MOYO WAKE WANDALE

Za chidwi cha Lazarus Chakwera chofuna kuyima nawo ku convention ya MCP chidawululika pa 9 April, 2013 pamene mphekesera zidayamba kumveka m'matsamba amchezo, ndipo zidatsimikizika pa 14 April, 2013. Chakwera, adakapereka makalata ofuna kupikisana nawo pa convention_yo yomwe imayenera kuchitika pa 27 April, koma idasinthidwa kupita pa 10 mpaka 11 August m'chaka chomwecho cha 2013, kumene iye adasankhidwa kudzayimilira chipani cha MCP pa zisankho za mu 2014. Iye adalowa m'malo mwa Dr. John Tembo, yemwe adali mtsogoleri wachipanicho asadabwera Chakwera.

Chakwera adalengedza kutula pansi udindo wa utsogoleri wampingo wa Malawi Assemblies of God pa 14 May, 2013. Chakwera poyankhula pake anati iye anachita kuyitanidwa ndi Mulungu kuti atumikire gulu la anthu ambiri (that's Malawi) osati kagulu ka anthu ochepa omwe uli mpingo ochepa. Ndipo atawona masomphenya awa Chakwera anawerenga Exsodo chapter 3 ndipo atamaliza kuwerenga chapter ichi iye anasimikizika mtima kuti azatumikira a Malawi tsiku limozi.

Chitangochitika chisankho cha mu 2014, Professor Peter Mutharika wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) ndiyemwe adapambana. Mphekesera zidamveka kuti; zisankhozo sizidayende bwino, koma Lazarus Chakwera adayankhula kumtundu wa amalawi kuti; asunge bata ndi mtendere, komanso kuvomeredza zotsatira za zisankhozo, ndipo adikire zisankho zina zomwe zikubwera mtsogolo.
Kupatula kuti anakhalapo mtsogoleri wachipani chachikulu chotsutsa boma m'dziko la Malawi, Chakwera adaliso phungu wa nyumba yamalamulo woyimira dera la kumpoto chakumadzulo kwa boma la Lilongwe (Lilongwe North West Constituency).
.
Mu chaka cha 2018, Lazarus Chakwera adasankhidwanso ku convention ya chipani cha MCP, kuti ndiyemwe adzachiyimire pa mpando wa president pa zisankho zomwe ziichitike m'dziko la Malawi pa 21 May, 2019, ndipo adasankha "Sidik Mia" kukhala wachiwiri wake. Zisankho za 2019 zitachitika,zipani zitatu ndizo zinkapikisana kwambiri DPP,MCP ndi UTM ndipo masankho apatatu atachitika a Chakwera anathera pa #2 a Mutharika ndiwo analengezedwa kuti apambana ndi Justice Jane Ansah koma kulongosola kwa anthu ankati zisankhozo sizinali bwno chifukwa munachtka zochitika zambiri monga kugwilisidwa ntchito kwa Tippex ndi zina. A Mutharika atalengezedwa kuti apambana a Chakwera anachitisa msonkhano pa 31 May,2019 ndipo Iwo anayankhula izi;
.“Ine Lazarus Chakwera ndikunena pano kuti sindikugwirizana ndi zotsatira zomwe bungwe la MEC linalengeza. Ife tikasuma ku high court kuti chilungamo chiwoneke pa nkhniyi, khothi lilamule kuti zotsatirazi ndi zosavomerezeka ndipo agamule kuti zotsatirazi ndi zosavomerezeka, chisankho chichitikenso,” anatero Chakwera.
Chakwera anawonjezera kunenaso kuti “dziko lathuli kuti lidzuke, Mutharika akuyenera agwe.”
A Chakwera atayankhula izi sanachedwe ndipo anakasuma kukhoti kuti masankho sanayende bwno. Amzao a UTM mosogozedwa ndi President wao Saulosi Chilima nawoso anakasuma ndipo milanduyi anayiphatikiza ati inali yofanana. Ma bungwe osiyanasiyana anali akuyankhulaposo kuti zisankho sizinayende bwno ndipo bungwe lomeneyera anthu ufulu la HRDC linachitisapo ziwoneselo kwambiri kuti Jane Ansah akuyenela atule pansi udindo wake ati sanayendese bwno zisankho za pa 21 May,2019. A Chakwera ndi a Chilima atapeleka ma umboni onse chigamulo cha high court chinalipo pa 3 February,2020 pamene dziko lonse linali zii kukhala chidwi ndizosatira za Ku court. Ndipo pa chigamulo chomwe anapeleka ma judge Iwo ananena kuti zisankhodi za chaka chatha sizinayende bwno ndipo ananena kuti chaka chatha kunalibe zisankho komanso analamula kuti a Malawi akuyeneleka kuvotaso pasanathe masiku 150. Court linanenaso kuti owina pa masankhowa akuyeneleka kuzawina ndi 50+1%,kusonyeza kuti owina azawine ndi theka lamavote. Pa chigamulo ichi zinapangsa kuti a Chilima abwerere u vice President wadziko lino komanso pakhale masankho a sopano. Chipani cha DPP sichinakhutire ndichigamulochi ndipo linakasuma Ku court lalikulu la Supreme yomwe inagamula mu April ndipo chigamulo chake sichinasiyane ndi cha high court. A Supreme Court anawonjezera kunenaso kuti anthu ovota akhale aja anavota mu 2019 chifukwa panali ma report kuti a DPP akulembesa ana kuti azavote.

Pa chigamulo cha Ku court chija cha 50+1% zinapangsa kuti payambe kumveka mphekesera kuti UTM ndi MCP akufuna kupanga mgwirizano ndipo izi zinathekadi MCP ndi UTM anapanga mgwirizano omwe anawutcha tonse alliance womwe umanyamula zipani pamodzi 9 (zina PP,AFORD,Mafunde etc). Chimozimoziso chipani cholamula cha DPP chinapanga alliance ndi UDF called DPP/UDF Alliance. Tonse Alliance inasankha a Chakwera kuti ndwo atasogolere mgwirizano wao koma a Mec anagwilisa ntchito MCP ndi logo yawo ndipo sanagwilise dzina la Tonse alliance. Pomwe DPP/UDF alliance inasankha a Peter Mutharika kuti asogolere mgwirizano wao. Ma paper oyimila u President anapelekedwa Ku MEC cha mu May ndipo zinasimikizika kuti Tonse alliance,DPP/UDF alliance komanso Mbakuwaku movement ndiwo atapikisane masankho a u president date lomwe linatchulidwa pa 23 June aphungu atasankha. A Chakwera popeleka ma paper anasankha a Chilima ngati runningname wao.
“God has given us Dr Chilima whose courage has confronted this disease and answered the call to cure it on behalf of Malawians, and that is destiny,” said Chakwera.

Tonse alliance inapanga campaign wapamwamba kwambiri chifukwa inayenda kwambiri pafupifupi madera onse Malawi muno chimozimozi DPP/UDF alliance anayesesa mbaliyawo. Kumayambiliro a June, DR Jane Ansah anatula pansi ngati chair commission wa Mec zomwe zinakondwelesa a Malawi ambiri ndipo Justice DR Chifundo Kachale ndwo analowa mmalo mwa Jane Ansah. Masankho anachtka pa 23 June ndipo anthu atavota zosatira zinatuluka pa 27 June zomwe zinawonesa kuti a Chakwera ndiwo apambana. A Chakwera analengezedwa kuti apambana ndi 58% pa mavote 4.4 million omwe anaponyedwa ndipo anthu 2.6 million anavotera MCP. A Mutharika omwe anali a President anathera pa #2. Ndipo Mwambo olumbilisa unachitika pa 28 June,2020 ndipo a Chakwera anati
"Tikufuna Malawi okomela onse,Malawi osayang'ana chigawo,nonse amene zakuvutani pepani koma ndkulonjezani kuti sindkukhumudwisani ndigwira nanu ntchito limozi tipange Malawi wasopano,Malawi wokomela tonse"
.
MOYO WAKE WA BANJA.

Lazarus Chakwera ndiwokwatira. Adakwatira mkazi wotchedwa "Monica Gondwe" omwe ati anakumana nthawi yomwe anali ku Unirvesity nthawiyo a Chakwera ali ku Chanco ndipo a Monica ali ku Polytechnic. Monica kwao ndi ku Rumphi ndipo adabereka naye ana anayi (4); ndipo mayina awo ndi: Nicky, Violet, Tapiwa, ndi Marlyn.
 

Chakwera anthu amamuziwa ngati munthu odekha osakonda zolakhulalakhul
a,munthu owopa Mulungu,munthu okwanilisa lonjezo lake komanso munthu okonda anthu osayang'ana mbali. Chinaso chodabwsa ndi chakuti a MEC atanena kuti a Chakwera apambana a Chakwera asayambe kunyadila anayamba Kaye kupemphera kuthokoza Mulungu ndipo post yawo yawo pa page pa FB Iwo anati "Zikomo ambuye wanga,Yesu" zomwe zikupasa anthu chiyembekezo kuti President ameneyi ndiwoopa Mulungu ndipo akwanisa zofuna zawo. Chakwera akhala President wa number 6 wadziko la Malawi ndipo alamulira kwa zaka zisanu 2020-2025.. A Chakwera amakondaso mpira ndipo amasapota Mighty Be forward Wanderers komanso Arsenal.

Image

***

0
LOL
2
LOVED
0
PURE
0
AW
0
FUNNY
0
BAD!
0
EEW
0
OMG!
0
ANGRY
0 ***