ULEMELERO WA ACHINYAMATA ULI MU MPHAMVU ZAWO

Achinyamata a mpingo wa Anglican ku Salima, anasonkhana pamodzi kwa masiku atatu kuyambila pa 25 mpaka pa 27 april 2025, pankumano wa achinyamata omwe unachitikila ku Chipoka Parish.

نشر  723 الآراء محدث منذ 5 الشهور

Achinyamata a mpingo wa Anglican ku Salima, anasonkhana pamodzi kwa masiku atatu kuyambila pa 25 mpaka pa 27 april 2025, pankumano wa achinyamata omwe unachitikila ku Chipoka Parish.  Nkumanowu, unachitika pa mutu woti “ulemelero wa achinyamata uli mu Mphamvu zawo” omwe ukuchokela pa buku la Miyambo chapter 20 verse ya 29. Nkumanowu umalimbikisa achinyamata kugwiritsa ntchito mphamvu ndi mphatso zomwe alinazo popeleka ulemelero kwa Mulungu.
 

Image

Kwa masiku atatu, achinyamatawa aphunzitsana zinthu zosiyanasiyana zolimbikitsa chikulupirilo chawo, kuchita mipikisano yolimbikitsa mawu a mulungu komanso kuchita masewero osiyanasiyana polimbikitsa umodzi ndi chinzake pakati pawo.

Achinyamata ambiri omwe anali ku nkumanowu, ati nkumanowu waathandiza kukula muuzimu komanso aphunzila kufunika kogwiritsa ntchito mphamvu za pauchinyamata popititsa ntchito yofalitsa mawu a Mulungu patsogolo komanso polemekeza Chauta.

Ngati mbali imodzi yoonetsa chikhulupiliro chawo muzi chitochito, achinyamatawa anakasesa ku Chipatala cha Chipoka, poonetsela chikondi, chisamaliro ndi udindo kwa onse.

Ven. Chalemba kutsogolera mwambo wamapemphero

Image

Atsogoleri a mpingowu ayamikila nkumanowu ponena kuti wathandiza achinyamata kukhala odalira mawu amulungu komanso ochita mawuwa poonetsa zintchito, umodzi ndi chikondi zomwe ndi m’dalitso ku mpingowo.
Nkumanowu inali njira imodzi yothandiza achinyamata podzipeleka kwa yesu khristu komanso kuzikonzekeletsa muuzimu pamene akukula.

 

Image

Ena mwa maphunziro omwe achinyamatawa anaphunzitsana ndi okhuza biziness komanso ukhondo kwa wachinyamata.
Pamene Nkumanowu umapita kumalecheleche, zinaonetsatuh kuti ndizotheka komanso ndizoona kuti pamene wachinyamata wayima muchikukhulupiliro, mphamvu zake zimakhala nyali yowalitsa dziko lapansi kuonetselatu kuti ulemelero wa achinyamata ulidi mu mphamvu zawo.


ردة فعلك؟

0
LOL
1
LOVED
0
PURE
0
AW
0
FUNNY
0
BAD!
0
EEW
1
OMG!
0
ANGRY
0 تعليقات