Download Robert Chiwamba - Mbiri Safuta
										MBIRI SAFUTA 
 
Ngwazi Prof. Bingu wa Mutharika adali wakulu 
 
Olo utapita kunja nkhani yake ukayipeza 
Kutseka maso ako pogona mbiri yake ukayilota 
Kuthawira kumaiko akutali, m'mabuku akumeneko za masomphenya ake ukazikumana 
Mbiri yadziko lino ndi sanza opanda malemu Professor Bingu wa Mutharika,  
Ngwazi yachiwiri ya pfuko la Nyasaland, chitsulo chanjanji, nthetsa makani anzungu Katswiri. 
 
Anayankhulako m'modzi mwa atsogoleri athu padzana 
Kuti vuto la Amalawi ambirife sitichedwa kuyiwala 
Koma lero pamene tukumbukira Mapwiya Mulhupale sindikulorani kuti muyiwale 
Kuti mukangosamba nkulowa munsewu wa Chitipa Karonga mwalowa mu ntchito za manja ake 
Ndithu mukangopenya munthu akudumphadumpha amusankhira ku MUST dziwani akujowelajowela zipatso za mifuleni ya thukuta lake 
Akangoti ndimagwira ntchito kunyumba yamalamulo dziwani amabindikira mu nyumba zomwe anamanga ndi luntha lake 
 
Nsanje sachitira akufa, mbiri ilibe Dastala, M'kunena kwa achinyamata alero Ngwazi Professor Lorani ntchito za manja anga zindichitire umboni aja anali dada 
 
Anamangira Kamuzu nyumba yogonamo kwamuyaya yaulemu 
Uku timakuti chitsulo kulemekeza chitsulo chinzake 
Sanamvere Mzungu pomukaniza kuyambitsa feteleza otchipa, anamuyambitsa njala yonse balala 
Uku timakutcha kudziwa chomwe ukuchita 
Potumbwa Edzi anagawa ma ARV aulere imfa zodza ndi iyo Red Card Lakata 
Uwu timautcha utsogoleri okonda anthu  
 
Ngwazi Professor tiyende pamodzi ndi mtima umodzi aja sanali size yanu 
Ngwazi Professor  Bingu Wamutharika uja sungamamuyerekeze ntatsogoleri tamabungwe tongopanga phokoso mmawayilesiti 
Ngwazi Prof. belu suyimba uli pakaliyala aja mbewu yawo anasiya kupanga 
 
Moti ndunena pano sindingayiwale kuwauza ana anga kuti chinasesa mavote Chitipa to nsanje chokhachokha  ana amuna bambo 
Zonse ndege ndi ma tractor a green belt zinasowetsedwa zija zinali thukuta la kulimbika mtima kwake akatundu bwana 
Mayi anu achira? Kuchipatala cha Nkhotakota kaya Nkhatabay wo achilira mu nyumba zomwe anamanga kudzera mmasomphenya ake 
 
Ndale tazisiyani, ufiti musamatambe masana, nsanje sachitira akufa perekani ulemu kwa Professor Bingu Katakwe 
 
Anagumula nyumba zonse zomangidwa mosatsata malamulo, kuthamangitsa ma vendor munsewu, kukana mathanyula kuliri kuveka ma driver ndi ma conductor a ma minibus Uniform 
 
Uku timakutcha kuswa kuswa 
 
Tutitu anathotha Kazembe wa angerezi, kukana kugwetsa mphavu yakwacha, kulili kuopseza kuti athamangitsa timakampani togula fodya, fodya kukweleratu mtengo 
 
Uku timakuti kusenda kusenda 
 
Eish anawauza apolisi wakuba wamfuti Shoot to Kill umbava onse thii lakata 
Uwu timautcha utsogoleri wachitetezo 
 
Ngwazi Professor Shoot to Kill aja anali mfumu ya kuswa kuswa 
Ngwazi Prof uja monga inenso ankadziwa kuti apolisi ngofunikira osamawaphweketsa 
Ngwazi achiwiri aja anali makolo 
 
Zofooka mu ulamuliro wawo osalephera mwana okonzedwa pa Poly, kulili anthu otsogozedwa kulichete pa 20 July 
 
Pepani olira pepani 
 
Zolakwika zinalipodi, anyamata achipani ozungulira ndi zikwanje, mafuta, shuga, magetsi ndalama zakunja kusowa  
koma ndindani amene anabadwa mwankazi alibe zofowoka ndiyankheni?  
 
Ulamuliro wa Ngwazi Prof. Bingu Wa Mutharika sunali wa angelo 
Ngwazi Prof Bingu Wa Mutharika monga inuyo ndi akazanuwonso anali ndi zofooka 
Zofowoka za Ngwazi Prof Bingu Wamutharika zinali zochepa tikayerekeza ndi chake chitukuko komabe sitingazipeputse pepani olira pepani 
 
Nde lero pamene zilumika zapitapo chipezereni ufulu ozisaukitsa tokhawu 
Nduti lero, pamene amalawi ambiri akubadwabe kukula mpaka kufa mumdima wa umphawi wadzaoneni 
Sitingayiwale  Professor Bingu wa Mutharika Malemu 
Limodzi ndi makosana ena amene anayesetsako kuyasa nyali mumdima wathu 
Achina Mayi Anastanzia Msosa ndi mayi Ethel Mutharika Malemu.  
Bwana Dr. Chifundo Kachali ndi bambo Nyakwawa Usiwa Usiwa malemu 
Zikomo chifukwa cha chilichonse munachitira Malawi 
Yakanika ndakatulo kufotokoza zonse  zitukuko za Ngwazi yachiwiriyi zachulukitsa 
Koma ngati pali tsache, ninkheni nkasese  mwaulemu kumpumulo wabata 
Ngati pali chitchetcho patseni nkatchetche panyumba yotsiriza yabambo pasamele udzu 
Chitsime chimadziwikadi kuya madzi pouma 
Ngwazi Professor Bingu Wa Mutharika uja ankatikonda 
Ngwazi prof Bingu uja sitinamumvetse 
Ngwazi Prof. Bingu uja adali wakulu 
Mbiri safuta.									
