Published 2 years ago in Poem's
malawitunesads malawitunesads malawitunesads malawitunesads
  • 522
  • 1,101
  • 1
  • 0
  • 5
  • 0
  • 0

Download: Raphael Sitima - Pemphero Feat Voice of Brothers

Lyrics

PEMPHERO.

Baba,Mulungu wanga.
Kaba chitsa kavina katopa.
Katela kauluka kalema.
Ndikuvutikatu n'kudwala ine.
Chikhala n'fukabondo,
Abalewa akadandisakira mtera ndidziwa.
Chikhala ndi maso okhawa awawa,
Kapena mutu wa namtongwe,
Opwetekera kuchibumi.
Anthuwa akadandifunira madzi a nkhunda.
Chikhala n'kuchepa kwa magazi,
N'kadakuuzani mtimawu ukuthawathawa.
Nokha mukadaonera kupukutiwa anga mmera pa nsonthi.
Chikhala ndi malungo yawa.
Mukadapenyera bvikulo wachikaso.
Kodi n'chifuwa chokoka mtima?
Chilavulitsa magazi n'chiyani n'kamakhobola.
Onditama,ondichemelera andipaka phula.
Moyo ndaudziwa lero.
Zokhumba zake ndi mtolo.
Zina zokuyezeka wekha pa ulimbo.

Onditsina khutu.
Onditsanulira malango.
Ondiuza kuti mphwanga umenewu simoyo ukupangawu,
Sankadula mlomo pa ine.
Sindikudziwa chidandiona n'chiyani?
Chondikodolera ku maphwando,
Ofupikitsa moyo chotere.
Udolo pa chiwerewere.
Asapaze wamalichaje mtsikana,
Ovala ndekesha zamberewere.
Asanyamule chiphsephse mwana wamkazi.
Anga sizinamtole oba dzuwa lili khee!!
Ine mtima phakuphaku konko kwa namwali.

Uchidakwa wa ziyalu.
Kusuta ndi mankhwala ozunguza bongo.
Kani n'zoonadi sizikuti leke za padziko?
Chisenjesenje chautsa chiseyeye lero.
Mwa njovu sindidzayetsanso mosewera mphetchepetche.
Kani ndi mwala wa ndere moyowu?
Kuuchitira zibwana basi watelereka moyo.

Sindingakane ine Chauta kuthamboko.
Onena ankati;
"Mukusewerapo ndi ndi pamsampha amwene."
Ine koma makani kusamva.
Nimati ofa lero safa mawa!!
Chibwana changa chandisandutsa bwenzi la chipatala lero.
Ali kwaani anzanga ndinkanyada nawo nanditama?
Atsikana ziphadzuwa ndinkasimbwa nawo aja,
Sindikudziwa ali mtunda uti pano?
Mbiri yanga ikhale phunziro kwa ena lero.

Pano ndidza kwa inu
Ndi mtima onyonyomala.
Leza,Mphambe ,Chiothamisi.
Inu amene liwu lanu likanganula mtunda ndi nyanja,
Linasiyanitsa moyo ndi imfa.
Kopanda inu palibe kangachite mafulukutu pa dzikoli.
Mundilengere mtima wa siteki lero,
Ndikukunkhunula chimtima cha dwale.
Ichi chosamva mlango wa ena.

:
/ :

Queue

Clear