Published 4 years ago in Poem's
malawitunesads malawitunesads malawitunesads malawitunesads
  • 1,025
  • 2,144
  • 1
  • 0
  • 21
  • 0
  • 0

Ndakatulo yotopa ndim'chitidwe wa anthu osazindikira kuti anthu amatopa

Lyrics

Anthutu amafika potopa
Kungotopa basi kuti tatopa tangotopa
Ukuku n'kutopa basi tatopa ife
Anthu amafika potopa
Akatopa anthu saopa mfuti
Amamuuza mwini unyolo omba mfuti yako sitisuntha
Kaya upha khumi ipha wachikhumi nchimodzi ndiwe
Mfuti ili paphewa osaka amasanduka osakidwa
Mbaula kuyisiya kuthawa wapansi anthu ali pambuyopo mawowowo
Omutuma atafuchilila pakona wefuwefu thukuta m'mwezi ozizira
Taziona ndi maso ife
Anthu amafika potopa
Anthutu amatopa
Kungotopa basi kuti eish tatopa ifeyo tangotopa ukuku nkutopa tatopa amwene basi kutopa
Anthu amafika potopa
Anthu akafika potopa zamtundu amazitaya kutali
Ukamadya wekha ndi achanzako ndalama zomwe zimayenera kukhala zagulu amangokuyang'ana
Ukamasimbwa kumaopseza anthu kuntchito mudzina lachipani mtundu kaya chipembedzo amangokupenya
Ukamalalata ngati unaperekera matope pomanga phiri lamulanje kapena Mchenga wa mmbali mwanyanja poumba nyanja ya Malawi amangoti okhe
Kenaka anthu amatopa
Kungotopa basi kuti amwene tamutopera bwana wausilu uyu tatopa ife kungotopa basi ukuku nkutopa basi tatopa eish
Anthu amafika potopa
Akatopa madhilu ako onse amangowulula
Kugwirizana kuti mube aka ena kukuwululani
Kuika anyamata anu achifwamba kuti akafwambe osiyana nanu maganizo anthu kuwagwira nkuwabandula iwo kulira mayoooooooo
Kuyesera kumema abale ako akhale yako mbali iwo toto bola kuthandiza wadela
Anthu amatopa
Bwana ku offesiko ma Juniyo amatopa
Kungotopa basi kuti agh tatopa tingowawazako bwanawa khofi chichitike chichitike tatopa
Osamasewera ndi anthu bwana ku ofesiko
Anthu amatopa
Nde paulo anati ngati mungathe khalani pamtendere ndi aliyense
Anthu amatopa
Musadye ndalama zamisonkho yawanthu magalimoto mbwembwembwe akamadandaula inu fyoko fyoko kumayankhanso za mwano
Anthu amatopa
Osaopseza anthu osiyana nanu maganizo mtidzi kumangokhala wa okulambirani okha
Anthu amatopa
Kuwafinya ma Juniyo pantchitopo kuwafinya majuniyo bwana kulira pyeee mukulalata ngati ndinu amuyaya
Anthu amatopa
Ana anu omwe, abale anu omwe, akazanu omwe amunanu eni eniwa, wantchito wapakhomoyu, mukamapitiriza kuwasimbwira mumachita kuja nyekhwe adzakuonetsani ndi iwo tsiku ndilimodzi
Anthu amatopa
Kulikonse mupite msaiwale ichi choti khalidwe ndi chuma, nthawi nkachitsilu
Anthu amafika potopa
Mufuniranjinso umboni wina
Ndatopa nane ndatopa ndiyigoneke pompa ndakatuloyi
Nde usavutike kundiyimbilanso phone kumandiuza zopusa zandakatuloyi
Ndingokuuzilatu ndikuyenda otopa topa monga aMalawi ambiri
Anthu amatopa

:
/ :

Queue

Clear